6. Nagona Basa ndi makolo ace, naikidwa ku Tiriza; ndipo Ela mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.
7. Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Basa ndi nyumba yace, cifukwa ca zoipa zonse anazicita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wace ndi macitidwe a manja ace, nafanana ndi nyumba ya Yerobiamu; ndiponso popeza anaikantha.
8. Ndipo caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi ca Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Basa analowa ufumu wa Israyeli ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri.
9. Ndipo mnyamata wace Zimri, ndiye woyang'anira dera lina la magareta ace, anampangira ciwembu; koma iye anali m'Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba m'Tiriza.