47. Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomo lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wace wacifumu upose mpando wanu wacifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo.
48. Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israyeli, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wacifumu, maso anga ali cipenyere.
49. Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anacita mantha, nanyamuka, napita yense njira yace.
50. Ndipo Adoniya anaopa cifukwa ca Solomo, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe.
51. Ndipo anthu anakauza Solomo, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomo, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomo alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wace ndi lupanga.