33. Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomo mwana wanga pa nyuru yanga yanga, nimutsikire naye ku Gihoni.
34. Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israyeli; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.
35. Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wacifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa lsrayeli ndi Yuda.
36. Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.