8. Cifukwa cace iye wotaya ici, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wace Woyera kwa inu.
9. Koma kunena za cikondano ca pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzace;
10. pakutinso munawacitira ici abale onse a m'Makedoniya lonse. Koma tikudandaulirani, abale, mueurukireko koposa,
11. ndi kuti muyesetse kukhala cete ndi kucita za inu eni ndi kugwira nchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;
12. kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.
13. Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe ciyembekezo.
14. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi iye iwo akugona mwa Yesu.