40. Palinso matupi am'mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam'mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso.
41. Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m'ulemerero.
42. 9 Comweconso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'cibvundi, liukitsidwa m'cisabvundi;
43. 10 lifesedwa m'mnyozo, liukitsidwa m'ulemerero; lifesedwa m'cifoko, liukitsidwa mumphamvu;
44. lifesedwa thupi Iacibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi Iacibadwidwe, palinso lauzimu.