13. Sicinakugwerani inu ciyeso koma ca umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi ciyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
14. Cifukwa cace, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.
15. Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu cimene ndinena.
16. Cikho ca dalitso cimene tidalitsa, siciri ciyanjano ca mwazi wa Kristu kodi? Mkate umene tinyema suli ciyanjano ca thupi la Kristu kodi?