6. Ndipo pamene mukadya, ndi pamene mukamwa, mukadya si ndinu, mukamwa si ndinu kodi?
7. Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'midzi mwace pozungulira pace, ndi m'dziko la kumwela, ndi m'cidikha munali anthu okhalamo?
8. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Zekariya, ndi kuti,
9. Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani ciweruzo coona, nimucitire yense mnzace cifundo ndi ukoma mtima;