9. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,
10. Tenga a iwo a kundende, a Keledai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe ku nyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kucokera ku Babulo,
11. ndipo utenge siliva ndi golidi, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkuru wa ansembe;