Zefaniya 1:17-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu a'khungu, popeza anacimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati pfumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.

18. Ngakhale siliva wao, ngakhale golidi wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yace; pakuti adzacita cakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.

Zefaniya 1