Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ace ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala copulumukirako anthu ace, ndi linga la ana a Israyeli.