Yoswa 19:32-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Maere acisanu ndi cimodzi anaturukira ana a Nafitali, ana a Nafitali monga mwa mabanja ao.

33. Ndipo malire ao anayambira ku Helefi, ku thundu wa ku Zaanani, ndi Adaminekebi, ndi Yabineeli, mpaka ku Lakumu; ndi maturukiro ace anali ku Yordano;

34. nazungulira malire kumka kumadzulo ku Azinotu-tabori, naturukira komweko kumka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Aseri kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordano kum'mawa.

35. Ndipo midzi yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti;

36. ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori;

37. ndi Kedesi, ndi Edrei, ndi Eni-hazori;

38. ndi Ironi, ndi Migidala-eli, Horemu, ndi Betianati, ndi Beti-semesi; midzi khumi ndi isanu ndi inai, ndi miraga yao.

39. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Nafitali, monga mwa mabanja ao, midzi ndi miraga yao.

40. Maere acisanu ndi ciwiri anaturukira pfuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao.

41. Ndipo malire a colowa cao anali Zora, ndi Esitaoli ndi Iri-semesi;

42. Saalabini, ndi Aijaloni ndi ltila;

43. ndi Eloni ndi Timna ndi Ekroni;

44. ndi Eliteke, ndi Gibetoni, ndi Baalati;

45. ndi Yehudi, ndi Bene-beraki, ndi Gatirimoni;

46. ndi Me-jarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pajapo.

47. Koma malire a ana a Dani anaturuka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, naucha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao.

48. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miraga yao.

49. Ndipo atatha kuligawa dziko likhale colowa cao monga mwa malire ace, ana a Israyeli anapatsa Yoswa mwana wa Nuni colowa pakati pao;

50. monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mudzi umene anawapempha, ndiwo Timinatisera, ku mapiri a Efraimu; ndipo anamangamudziwonakhala m'mwemo.

51. Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazare wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli, zikhale zao zao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la cihema cokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.

Yoswa 19