15. Ndipo mbali ya kumwela inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; naturuka malire kumka kumadzulo, naturuka kumka ku citsime ca madzi a Nefitoa;
16. natsikira malire kumka polekezera phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca mwana wa Hinomu, ndico ca m'cigwa ca Refai kumpoto; natsikira ku cigwa ca Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwela, natsikira ku Enirogeli;
17. nalembedwa kumka kumpoto, naturuka ku Eni-semesi, naturuka ku Gelilotu, ndiwo pandunji pokwerera pa Adumi; natsikira ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;
18. napitirira ku mbali ya pandunji pa Araba kumpoto, natsikira kumka ku Araba;