Yoswa 15:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. nakwera malire kumka ku Dibiri, kucokera ku cigwa ca Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa cikweza ca Adumi, ndiko kumwela kwa mtsinje; napitirira malire kumka ku madzi a Enisemesi, ndi maturukiro ace anali ku Eni-rogeli;

8. nakwera malire kumka ku cigwa ca mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwela, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kumka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ace a cigwa ca Refai kumpoto,

9. Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka citsime ca madzi ca Nefitoa, naturukira malire ku midzi ya phiri la Efroni; ndipo analemba malire kumka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.

10. Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kumka kumadzulo, ku phiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Beti-semesi, napitirira ku Timina;

11. naturuka malire kumka ku mbali ya Ekroni kumpoto; ndipo analemba malire kumka ku Sikeroni, napitirira ku phiri la Baala, naturuka ku Yabindi; ndipo maturukiro a malire anali kunyanja.

12. Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikuru ndiwo malire ace. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.

13. Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.

14. Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.

Yoswa 15