1. Ndipo gawo la pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku cipululu ca Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.
2. Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mcere, ku nyondo yoloza kumwera;
3. naturuka kumwela kwa cikweza ca Akarabi, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Barinea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;