7. Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israyeli anawakantha tsidya lija la Yordano kumadzulo, kuyambira Baala-gadi m'cigwa ca Lebano mpaka phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mapfuko a Israyeli, likhale lao lao, monga mwa magawo ao;
8. kumapiri ndi kucigwa, ndi kucidikha, ndi kumatsikiro, ndi kucipululu, ndi kumwela: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi:
9. mfumu ya ku Yeriko, imodzi; mfumu ya ku Ai, ndiwo m'mbali mwa Beteli, imodzi;
10. mfumu ya ku Yerusalemu, imodzi; mfumu ya ku Hebroni, imodzi; mfumu ya ku Yarimutu, imodzi;
11. mfumu ya ku Lakisi, imodzi;