Yoswa 1:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako.

10. Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti,

11. Pitani pakati pa cigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordano uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanu lanu.

Yoswa 1