7. Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kucita monga mwa cilamulo conse anakulamuliraco Mose mtumiki wanga; usacipambukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukacite mwanzeru kuli konse umukako.
8. Buku ili la cilamulo lisacoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kucita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzacita mwanzeru.
9. Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako.
10. Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti,