Yona 4:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Koma Mulungu anauikira mphanzi pakuca m'mawa mwace, ndiyo inadya msatsi, nufota.

8. Ndipo kunali, poturuka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wace wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.

9. Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima cifukwa ca msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.

10. Ndipo Yehova anati, Unacitira cifundo msatsiwo umene sunagwirapo nchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;

Yona 4