10. Ndipo Yehova anati, Unacitira cifundo msatsiwo umene sunagwirapo nchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;
11. ndipo sindiyenera Ine kodi kucitira cifundo Nineve mudzi waukuru uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?