Yona 2:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wace ali m'mimba mwa nsombayo.

2. Ndipo anati,Ndinaitana Yehova m'nsautso yanga,Ndipo anandiyankha ine;Ndinapfuula ndiri m'mimba ya manda,Ndipo munamva mau anga.

3. Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja,Ndipo madzi anandizinga;Mapfunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.

4. Ndipo ndinati, Ndatayika ndicoke pamaso panu;Koma ndidzapenyanso Kacisi wanu wopatulika.

5. Madzi anandizinga mpaka moyo wanga,Madzi akuya anandizungulira,Kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu.

6. Ndinatsikira ku matsinde a mapiri,Mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha;Koma munandikwezera moyo wanga kuucotsa kucionongeko, Yehova Mulungu wanga.

7. Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukila Yehova;Ndi pemphero langa linafikira Inu m'Kacisi wanu wopatulika.

8. Iwo osamalira mabodza opanda paceAtaya cifundo cao cao.

Yona 2