Yohane 8:52-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

52. Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi ciwanda. 10 Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa ku nthawi yonse.

53. Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?

54. Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli cabe; 11 Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za iye, kuti ndiye Mulungu wanu;

55. ndipo 12 inu simunamdziwa iye; koma Ine ndimdziwa iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa iye, ndidzakhala wonama cimodzimodzi inu; koma ndimdziwa iye, ndipo ndisunga mau ace.

56. 13 Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona, nasangalala.

57. Ayuda pamenepo anati kwa iye, Simunafikire zaka makumi asanu, ndipo munaona Abrahamu kodi?

Yohane 8