Yohane 7:38-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Iye wokhulupirira Ine, monga cilembo cinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kuturuka m'kati mwace.

39. Koma 1 ici anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, cifukwa Yesu sanalemekezedwa panthawi pomwepo.

40. Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena, 2 Mnene riyo ndi uyu ndithu.

41. Ena ananena, 3 Uyu ndi Kristu, Koma ena ananena, Kodi Kristu adza kuturuka m'Galileya?

42. 4 Kodi sicinati cilembo kuti Kristu adza kuturuka mwa mbeu ya Davine, ndi kucokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davine?

43. 5 Kudakhala tsono kusiyana m'khamulo cifukwa ca iye.

44. Koma 6 ena mwa iwo anafuna kumgwira iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja.

45. Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe akulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenga iye bwanji?

46. Anyamatawo anayankha, 7 Nthawi yonse palibe munthu analankhula cotero.

47. Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso?

48. 8 Kodi wina wa akuru anakhulupirira iye, kapena wa Afarisi?

Yohane 7