Yohane 5:35-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwace kanthawi.

36. Koma Ine ndiri nao umboni woposa wa Yohane; pakuti nchito zimene Atateanandipatsa ndizitsirize, nchito zomwezo ndizicita zindicitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.

37. Ndipo Atate wonditumayo, 1 Iyeyu wandicitira Ine umboni. Simunamva mau ace konse, kapena maonekedwe ace simunaona.

38. Ndipo mulibe mau ace okhala mwa inu; cifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo.

39. 2 Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundicitira Ine umboni ndi iwo omwewo;

40. ndipo 3 simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nao moyo.

41. 4 Ulemu sindiulandira kwa anthu.

42. Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe cikondiea Mulungu mwa inu nokha.

43. Ndadza Ine m'dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; akadza wina m'dzina lace la iye mwini, iyeyu mudzamlandira.

Yohane 5