20. Pakuti yense wakucita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe nchito zace.
21. Koma wocita coonadi adza kukuunika, kuti nchito zace zionekere kuti zinacitidwa mwa Mulungu.
22. Zitapita in anadza Yesu ndi akuphunzira ace ku dziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.
23. Ndipo Yohane analinkubatiza m'Ainoni pafupi pa Salemu, cifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.
24. Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende.
25. Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ace a Yohane ndi Myuda za mayeretsedwe.