1. Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lace Nikodemo, mkulu wa Ayuda,
2. Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wocokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kucita zizindikilo zimene inu mucita, ngati Mulungu sakhala naye,