Yohane 21:23-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Cifukwa cace mau awa anaturuka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananena kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli ciani ndi iwe?

24. Yemweyu ndiye wophunzira wakucita umboniza izi, ndipo analembera izi; ndipo tidziwa kuti umboni wace ndi woona.

25. Koma palinso zina zambiri zimene. Yesu anazicita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa. Amen.

Yohane 21