Yohane 20:29-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Yesu ananena kwa iye, Cifukwa wandiona Ine, wakhulupira; odala iwo akukhulupira, angakhale sanaona.

30. Ndipo zizindikilo zina zambiri Yesu anazicita pamaso pa akuphunzira ace, zimene sizinalembedwa m'buku ili;

31. koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupira mukhale nao moyo m'dzina lace.

Yohane 20