Yohane 2:15-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anaturutsa onse m'Kacisimo, ndi nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome;

16. nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Cotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.

17. Akuphunzira ace anakumbukila kuti kunalembedwa, Cangu ca pa nyumba yanu candidya ine.

Yohane 2