Yohane 18:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo m'mene anati kwa iwo, Ndine, anabwerera m'mbuyo, nagwa pansi.

7. Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? koma iwo anati, Yesu Mnazarayo.

8. Yesu anayankha, Ndati, Ndine; cifukwa cace ngati mufuna Ine, lekani awa amuke;

9. kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataya mmodzi.

Yohane 18