1. M'mene Yesu adanena izi, anaturuka ndi akuphunzira ace, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kedroni, kumene kunali munda, umene analowamo iye ndi akuphunzira ace.
2. Koma Yudasenso amene akampereka iye, anadziwa malowa; cifukwa Yesu akamkako kawiri kawiri ndi akuphunzira ace.
3. Pamenepo Yudase, m'mene adatenga gulu la asilikari ndi anyamata, kwa ansembe akulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.
4. Pamenepo Yesu, podziwa zonse zirinkudza pa iye, anaturuka, nati kwa iwo, Mufuna yani?