Yohane 12:5-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa cifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?

6. Koma ananena ici si cifukwa analikusamalira osauka, koma cifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amabazoikidwamo.

7. Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anacisungira ici tsiku la kuikidwa kwanga.

8. Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.

Yohane 12