Yohane 12:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pamenepo Mariya m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a nardo a mtengo wace wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ace ndi tsitsi lace; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wace wa mafutawo.

4. Koma Yudase Isikariote, mmodzi wa akuphunzira ace, amene adzampereka iye, ananena,

5. Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa cifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?

6. Koma ananena ici si cifukwa analikusamalira osauka, koma cifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amabazoikidwamo.

7. Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anacisungira ici tsiku la kuikidwa kwanga.

Yohane 12