1. Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paskha, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.
2. Ndipo anamkonzera iye cakudya komweko; ndipo Marita anatumikira; koma Lazaro anali mmodzi wa iwo akuseama pacakudya pamodzi ndi iye.
3. Pamenepo Mariya m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a nardo a mtengo wace wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ace ndi tsitsi lace; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wace wa mafutawo.