Yohane 11:45-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. Cifukwa cace ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Mariya, m'mene anaona cimene anacita, anakhulupirira iye.

46. Koma ena a mwa iwo anamuka kwa Afarisi, nawauza zimene Yesu adazicita.

47. Pamenepo ansembe akulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? cifukwa munthu uyu acita zizindikilo zambiri.

Yohane 11