Yohane 11:33-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, nabvutika mwini,

34. nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi iye, Ambuye, tiyeni, mukaone.

35. Yesu analira.

36. Cifukwa cace Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi!

37. Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sanakhoza kodi kucita kuti sakadafa ameneyunso?

Yohane 11