Yohane 10:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Onse amene anadza m'tsogolo mwa Ine ali akuba, ndi olanda: koma nkhosa sizinamva iwo.

9. Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulu-mutsidwa, nadzalowa, nadzaturuka, nadzapeza busa.

10. Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga, Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka.

11. Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wace cifukwa ca nkhosa.

12. Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa siziri zace za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;

13. cifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa.

14. Ine ndine Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira ine,

15. monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga cifukwa ca nkhosa.

Yohane 10