31. Ayuda anatolanso miyala kuti amponye iye.
32. Yesu anayankha iwo, ndakuonetsani inu nchito zabwino zambiri za kwa Atate; cifukwa ca nchito yiti ya izo mundiponya miyala?
33. Ayuda anamyankha iye, Cifukwa ca nchito yabwino sitikuponyani miyala, koma cifukwa ca mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu,
34. Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'cilamulo canu, Ndinati Ine, Muli milungu?
35. Ngati anawacha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo colemba sicingathe kutyoka),