Yohane 10:19-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda cifukwa ca mau awa.

20. Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi ciwanda, nacita misala; mukumva iye bwanji?

21. Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa ciwanda. Kodi ciwanda cikhoza kumtsegulira maso wosaona?

Yohane 10