33. Ndipo sindinamdziwa iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa iye, 9 yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.
34. Ndipo ndaona ine, ndipo ndacita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.
35. M'mawa mwacenso analikuimirira Yohane ndi awiri a akuphunzira ace;
36. ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, 10 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!
37. Ndipo akuphunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu.