Yohane 1:19-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayudaanatuma kwa iye ansembe ndi alembi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?

20. Ndipo anabvomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Kristu.

21. Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye, Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.

Yohane 1