19. Taona, ici ndico comkondweretsa panjira pace,Ndi panthaka padzamera ena.
20. Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro;Kapena kugwiriziza ocita zoipa.
21. Koma adzadzaza m'kamwa mwako ndi kuseka,Ndi milomo yako kupfuula.
22. Iwo akudana nawe adzabvala manyazi;Ndi hema wa oipa adzakhala kuli zi.