13. Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu;Ndi ciyembekezo ca onyoza Mulungu cidzatayika;
14. Kulimbika mtima kwace kudzatyoka,Cikhulupiriro cace cikunga nyumba ya tandaude.
15. Adzatsamira nyumba yace, koma yosamlimbira;Adzaiumirira koma yosakhalitsa.
16. Akhala wamuwisi pali dzuwa,Ndi nthambi zace ziturukira pamunda pace.
17. Mizu yace iyangayanga pa kasupe wamadzi,Apenyerera pokhalapo miyala.
18. Akamuononga kumcotsa pamalo pace,Padzamkana, ndi kuti, Sindinakuona.