Yobu 6:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Cimkomere Mulungu kundiphwanya,Alole dzanja lace lindilikhel

10. Pamenepo ndidzasangalala,Ndidzakondwera naco cowawa cosandileka;Pakuti sindinawabisa mau a Woyerayo.

11. Mphamvu yanga njotani kuti ndiyembekeze?Mathedwe anga ndi otani kuti ndipirire?

12. Kodi mphamvu yanga ndiyo mphamvu ya miyala?Mnofu wanga ndi mkuwa kodi?

13. Mulibe thandizo mwa ine ndekha; cipulumutso candithawa.

14. Iye amene akadakomoka, bwenzi lace ayenera kumcitira cifundo;Angaleke kuopa Wamphamvuyonse.

15. Abale anga anacita monyenga ngati kamtsinje,Ngati madzi a timitsinje akupitirira.

16. Amada cifukwa ca madzi oundana.M'menemo cipale cofewa cibisika;

17. Atafikira mafundi, mitsinje iuma;Kukatentha, imwerera m'malo mwao.

Yobu 6