Yobu 5:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Itana tsono; pali wina wakukuyankha kodi?Ndipo udzatembenukira kwa yani wa oyera mtimawo?

2. Pakuti mkwiyo umapha wopusa,Ndi nsanje imakantha wopanda pace.

3. Ndinapenya wopusa woyala mizu;Koma pomwepo ndinatemberera pokhala pace.

4. Ana ace akhala otekeseka, Napsinjika kucipata,Wopanda wina wakuwapulumutsa.

Yobu 5