16. Tapenya tsono, mphamvu yace iri m'cuuno mwace,Ndi kulimbalimba kwace kuli m'mitsempha ya m'mimba yace.
17. Igwedeza mcira wace ngati mkungudza;Mitsempha ya ncafu zace ipotana.
18. Mafupa ace akunga misiwe yamkuwa;Ziwalo zace zikunga zitsulo zamphumphu,
19. Iyo ndiyo ciyambi ca macitidwe a Mulungu;Wakuilenga anaininkha lupanga lace.
20. Pakuti mapiri aiphukitsira cakudya,Kumene zisewera nyama zonse za kuthengo,
21. Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi,Pobisala pabango ndi pathawale.