Yobu 38:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Analemba malire ace ndani, papeza udziwa?Anayesapo cingwe cace ndani?

6. Maziko ace anakumbidwa pa ciani?Kapena anaika ndani mwala wace wa pangondya,

7. Muja nyenyezi za m'mawa zinayimba limodzi mokondwera,Ndi ana onse a Mulungu anapfuula ndi cimwemwe?

8. Kapena anatseka nyanja ndani ndi zitseko,Muja idakamula ngati kuturuka m'mimba,

9. Muja ndinayesa mtambo cobvala cace,Ndi mdima wa bii nsaru yace yakulunga,

10. Ndi kuilembera malire anga,Ndi kuika mipikizo ndi zitseko,

11. Ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo;Apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?

Yobu 38