Yobu 36:20-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Musakhumbe usiku,Umene anthu alikhidwe m'malo mwao.

21. Cenjerani, musaluniike kumphulupulu;Pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa.

22. Taonani, Mulungu acita mokwezeka mu mphamvu yace,Mphunzitsi wakunga Iye ndani?

23. Anamuikira njira yace ndani?Adzati ndani, Mwacita cosalungama?

24. Kumbukilani kuti mukuze nchito zace,Zimene anaziyimbira anthu.

Yobu 36