Yobu 36:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma akapanda kumvera adzatayika ndi lupanga,Nadzatsirizika osadziwa kanthu.

13. Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo,Akawamanga Iye, sapfuulira.

14. Iwowa akufa akali biriwiri,Ndi moyo wao utayika ngati odetsedwa.

15. Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwace,Nawatsegulira m'khutu mwao mwa kupsinjika kwao.

Yobu 36