Yobu 31:23-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Pakuti tsoka locokera kwa Mulungu linandiopsa,Ndi cifukwa ca ukulu wace sindinakhoza kanthu,

24. Ngati ndayesa golidi ciyembekezo canga,Ndi kunena ndi golidi woyengetsa,Ndiwe cikhazikitso canga;

25. Ngati ndinakondwera popeza cuma canga ncacikuru,Ndi dzanja langa lapeza zocuruka;

26. Ngati ndalambira dzuwa lirikuwala,Kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;

27. Ndi mtima wanga wakopeka m'tseri,Ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;

Yobu 31