Yobu 3:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zi;Ngati makanda osaona kuunika.

17. Apo oipa aleka kumabvuta;Ndi apo ofoka mphamvu akhala m'kupumula.

18. Apo a m'kaidi apumula pamodzi,Osamva mau a wofulumiza wao.

19. Ang'ono ndi akulu ali komwe;Ndi kapolo amasuka kwa mbuyace.

20. Amninkhiranji kuunika wobvutika,Ndi moyo kwa iye wakuwawa mtima,

Yobu 3